4 Zinthu zimene mbozi zinasiya zinadyedwa ndi dzombe.+ Zimene dzombelo linasiya zinadyedwa ndi ana a dzombe oyenda pansi opanda mapiko ndipo zimene ana a dzombe oyenda pansiwo anasiya zinadyedwa ndi mphemvu.+
25 Ndidzakubwezerani mbewu za zaka zonse zimene dzombe ndi ana a dzombe oyenda pansi opanda mapiko, mphemvu ndi mbozi zinadya. Limeneli ndi gulu langa lankhondo lamphamvu limene ndinatumiza pakati panu.+