4 Mwina Yehova Mulungu amva mawu onse a Rabisake,+ amene mbuye wake mfumu ya Asuri yamutuma, kuti adzatonze+ nawo Mulungu wamoyo. Ndipo mwina amulanga chifukwa cha mawu amene Yehova Mulungu wanu wamva.+ Inuyo mupereke pemphero+ m’malo mwa otsalira amene alipo.’”+