Ezara 5:2 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 2 Panali pa nthawi imeneyi pamene Zerubabele+ mwana wa Salatiyeli+ ndi Yesuwa+ mwana wa Yehozadaki ananyamuka n’kuyamba kumanganso nyumba ya Mulungu. Nyumbayi inali ku Yerusalemu ndipo panali aneneri a Mulungu+ omwe anali kuwathandiza. Ezara 6:15 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 15 Iwo anali atamaliza kumanga nyumbayo pofika tsiku lachitatu la mwezi wa Adara,+ m’chaka cha 6 cha ulamuliro wa mfumu Dariyo. Zekariya 1:16 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 16 “Choncho Yehova wanena kuti, ‘“Ndithu ndidzabwerera ku Yerusalemu ndi kuchitira chifundo mzinda umenewu.+ Nyumba yanga idzamangidwa mmenemo,+ ndipo chingwe choyezera chidzatambasulidwa pa Yerusalemu,”+ watero Yehova wa makamu.’
2 Panali pa nthawi imeneyi pamene Zerubabele+ mwana wa Salatiyeli+ ndi Yesuwa+ mwana wa Yehozadaki ananyamuka n’kuyamba kumanganso nyumba ya Mulungu. Nyumbayi inali ku Yerusalemu ndipo panali aneneri a Mulungu+ omwe anali kuwathandiza.
15 Iwo anali atamaliza kumanga nyumbayo pofika tsiku lachitatu la mwezi wa Adara,+ m’chaka cha 6 cha ulamuliro wa mfumu Dariyo.
16 “Choncho Yehova wanena kuti, ‘“Ndithu ndidzabwerera ku Yerusalemu ndi kuchitira chifundo mzinda umenewu.+ Nyumba yanga idzamangidwa mmenemo,+ ndipo chingwe choyezera chidzatambasulidwa pa Yerusalemu,”+ watero Yehova wa makamu.’