Yesaya 58:4 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 4 Ndithu inuyo munali kusala kudya n’cholinga choti muzikangana, kulimbana,+ ndiponso kuti muzimenyana ndi nkhonya zovulaza.+ Kodi inuyo simunali kusala kudya n’kumaganiza kuti inali nthawi yoti mawu anu amveke kumwamba? Mateyu 6:16 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 16 “Pamene mukusala kudya,+ lekani kumaonetsa nkhope yachisoni ngati mmene onyenga aja amachitira. Iwo amaipitsa nkhope zawo kuti aonekere kwa anthu kuti akusala kudya.+ Ndithu ndikukuuzani, Amenewo akulandiriratu mphoto yawo yonse. Akolose 2:23 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 23 Ndithudi, zinthu zimenezo zimaonekera pa kulambira kochita kudzipangira, podzichepetsa mwachinyengo komanso pozunza thupi,+ ndipo zimaonekadi ngati zanzeru, koma n’zosathandiza kwa munthu polimbana ndi zilakolako za thupi.+
4 Ndithu inuyo munali kusala kudya n’cholinga choti muzikangana, kulimbana,+ ndiponso kuti muzimenyana ndi nkhonya zovulaza.+ Kodi inuyo simunali kusala kudya n’kumaganiza kuti inali nthawi yoti mawu anu amveke kumwamba?
16 “Pamene mukusala kudya,+ lekani kumaonetsa nkhope yachisoni ngati mmene onyenga aja amachitira. Iwo amaipitsa nkhope zawo kuti aonekere kwa anthu kuti akusala kudya.+ Ndithu ndikukuuzani, Amenewo akulandiriratu mphoto yawo yonse.
23 Ndithudi, zinthu zimenezo zimaonekera pa kulambira kochita kudzipangira, podzichepetsa mwachinyengo komanso pozunza thupi,+ ndipo zimaonekadi ngati zanzeru, koma n’zosathandiza kwa munthu polimbana ndi zilakolako za thupi.+