Deuteronomo 8:10 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 10 “Mukadzadya ndi kukhuta+ mudzatamandenso+ Yehova Mulungu wanu, chifukwa cha dziko labwino limene wakupatsani.+ 1 Samueli 9:13 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 13 Mukangolowa mumzinda, mum’peza ndithu asanapite kukadya kumalo okwezeka. Anthu sangayambe kudya pokhapokha iye atafika, chifukwa ndiye amadalitsa nsembeyo.+ Kenako oitanidwa amadya. Choncho pitani chifukwa mum’peza posachedwapa.” Mateyu 14:19 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 19 Kenako analamula khamu la anthulo kuti likhale pansi pa udzu. Pamenepo anatenga mitanda ya mkate isanu ija ndi nsomba ziwiri zija, n’kuyang’ana kumwamba ndi kupempha dalitso.+ Atatero ananyemanyema mitanda ya mkate ija n’kupatsa ophunzirawo, ndipo iwonso anagawira khamulo.+ Maliko 8:6 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 6 Ndiyeno anauza anthuwo kuti akhale pansi. Kenako, anatenga mitanda 7 ya mkate ija, ndi kuyamika.+ Atatero anainyemanyema n’kupatsa ophunzira ake kuti agawe, ndipo iwo anagawira khamu la anthulo.+
10 “Mukadzadya ndi kukhuta+ mudzatamandenso+ Yehova Mulungu wanu, chifukwa cha dziko labwino limene wakupatsani.+
13 Mukangolowa mumzinda, mum’peza ndithu asanapite kukadya kumalo okwezeka. Anthu sangayambe kudya pokhapokha iye atafika, chifukwa ndiye amadalitsa nsembeyo.+ Kenako oitanidwa amadya. Choncho pitani chifukwa mum’peza posachedwapa.”
19 Kenako analamula khamu la anthulo kuti likhale pansi pa udzu. Pamenepo anatenga mitanda ya mkate isanu ija ndi nsomba ziwiri zija, n’kuyang’ana kumwamba ndi kupempha dalitso.+ Atatero ananyemanyema mitanda ya mkate ija n’kupatsa ophunzirawo, ndipo iwonso anagawira khamulo.+
6 Ndiyeno anauza anthuwo kuti akhale pansi. Kenako, anatenga mitanda 7 ya mkate ija, ndi kuyamika.+ Atatero anainyemanyema n’kupatsa ophunzira ake kuti agawe, ndipo iwo anagawira khamu la anthulo.+