Yesaya 55:7 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 7 Munthu woipa asiye njira yake+ ndipo wopweteka anzake asiye maganizo ake.+ Iye abwerere kwa Yehova ndipo adzamuchitira chifundo.+ Abwerere kwa Mulungu wathu, pakuti amakhululuka ndi mtima wonse.+ Mateyu 6:12 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 12 Mutikhululukire zolakwa* zathu monga mmene ifenso takhululukira amene atilakwira.*+ Mateyu 18:22 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 22 Yesu anayankha kuti: “Ndikukuuza kuti, osati nthawi 7 zokha ayi, koma, Mpaka nthawi 77.+ Akolose 3:13 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 13 Pitirizani kulolerana ndi kukhululukirana ndi mtima wonse,+ ngati wina ali ndi chifukwa chodandaulira+ za mnzake. Monga Yehova* anakukhululukirani+ ndi mtima wonse, inunso teroni. 1 Petulo 4:8 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 8 Koposa zonse, khalani okondana kwambiri,+ pakuti chikondi chimakwirira machimo ochuluka.+
7 Munthu woipa asiye njira yake+ ndipo wopweteka anzake asiye maganizo ake.+ Iye abwerere kwa Yehova ndipo adzamuchitira chifundo.+ Abwerere kwa Mulungu wathu, pakuti amakhululuka ndi mtima wonse.+
13 Pitirizani kulolerana ndi kukhululukirana ndi mtima wonse,+ ngati wina ali ndi chifukwa chodandaulira+ za mnzake. Monga Yehova* anakukhululukirani+ ndi mtima wonse, inunso teroni.