Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Mateyu 17:20
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 20 Iye anawayankha kuti: “Chifukwa cha kuchepa kwa chikhulupiriro chanu. Pakuti ndithu ndikukuuzani, ngati mutakhala ndi chikhulupiriro chofanana ndi kanjere ka mpiru kuchepa kwake, mudzatha kuuza phiri ili kuti, ‘Choka pano upite apo,’ ndipo lidzachokadi. Palibe chimene chidzakhala chosatheka kwa inu.”+

  • Mateyu 21:21
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 21 Poyankha Yesu ananena kuti: “Ndithu ndikukuuzani, ngati mutakhala ndi chikhulupiriro, osakayika,+ mudzatha kuchita zimene ndachitira mkuyu umenewu. Komanso kuposa pamenepa, mudzatha kuuza phiri ili kuti, ‘Nyamuka pano ukadziponye m’nyanja,’ ndipo zidzachitikadi.+

  • Maliko 9:23
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 23 Yesu anafunsa bamboyo kuti: “Mukuti, ‘Ngati mungathe’? Chilichonsetu n’chotheka kwa aliyense ngati iyeyo ali ndi chikhulupiriro.”+

  • Maliko 11:23
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 23 Ndithu ndikukuuzani kuti aliyense wouza phiri ili kuti, ‘Nyamuka pano udziponye m’nyanja,’ ndipo sakukayika mumtima mwake, koma ali ndi chikhulupiriro kuti zimene wanena zichitikadi, zidzaterodi.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena