34 Zili ngati munthu amene anali kupita kutali kudziko lina,+ amene anasiya nyumba m’manja mwa akapolo ake, aliyense pa ntchito yake, ndi kulamula mlonda wa pachipata kuti azikhala maso.
36 Yesu anayankha kuti:+ “Ufumu wanga suli mbali ya dziko lino.+ Ufumu wanga ukanakhala mbali ya dziko lino, atumiki anga akanamenya nkhondo+ kuti ndisaperekedwe kwa Ayuda. Koma ufumu wanga si wochokera pansi pano ayi.”