32 Tsopano anapitiriza ulendo wawo wopita ku Yerusalemu. Yesu anali patsogolo pawo, ndipo iwo anadabwa kwambiri. Anthu amene anali kum’tsatirawo anayamba kuchita mantha. Pamenepanso anatengera pambali ophunzira 12 aja ndi kuyamba kuwauza zinthu izi zimene zinali pafupi kum’chitikira:+