38 Tsopano zitatha izi, Yosefe wa ku Arimateya, amene anali wophunzira wa Yesu koma wamseri chifukwa anali kuopa Ayuda,+ anapempha Pilato kuti amulole kuti akachotse mtembo wa Yesu, ndipo Pilato anamupatsa chilolezo.+ Choncho anafika ndi kuchotsa mtembowo.+