19 Munthu aliyense akamva mawu a ufumu koma osazindikira tanthauzo lake, woipayo+ amabwera n’kukwatula zomwe zafesedwa mumtima wa munthuyo. Izi ndi zofesedwa m’mbali mwa msewu zija.
21 Pakuti ngakhale kuti dziko mwa nzeru zake+ silinathe kumudziwa Mulungu,+ kunamukomera Mulungu mwa nzeru zake kupulumutsa okhulupirira kudzera mu nkhani yopusayo,+ imene ikulalikidwa.