58 Koma Petulo anali kumutsatirabe chapatali ndithu, mpaka anafika m’bwalo lamkati+ kunyumba ya mkulu wa ansembeyo. Atalowa mkatimo, anakhala pansi pamodzi ndi antchito a m’nyumbamo kuti aone zotsatira zake.+
54 Koma Petulo, anali kum’tsatira chapatali ndithu,+ mpaka anafika m’bwalo lamkati kunyumba ya mkulu wa ansembe. Kumeneko iye anakhala pansi pamodzi ndi antchito a m’nyumbamo, n’kumawotha moto walawilawi.