Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Levitiko 11:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 “‘Koma pakati pa nyama zimene zimabzikula ndi zimene zili ndi ziboda zogawanika, izi zokha musadye: Ngamila, chifukwa imabzikula koma ziboda zake n’zosagawanika. Nyama imeneyi ndi yodetsedwa kwa inu.+

  • Levitiko 11:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 “‘Pakati pa zolengedwa zouluka,+ izi zikhale zonyansa kwa inu. Siziyenera kudyedwa chifukwa ndi zonyansa: Chiwombankhanga,+ nkhwazi ndi muimba wakuda.

  • Levitiko 20:25
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 25 Muzisiyanitsa nyama yoyera ndi yodetsedwa, mbalame yodetsedwa ndi yoyera.+ Musadziipitse+ ndi nyama, mbalame kapena chilichonse choyenda padziko lapansi, chimene ine ndachipatula kuti musadye pogamula kuti ndi chodetsedwa.

  • Deuteronomo 14:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 “Musadye chinthu chilichonse chonyansa.+

  • Deuteronomo 14:19
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 19 Tizilombo tonse ta mapiko timene timapezeka tambiri n’todetsedwa kwa inu.+ Timeneti simuyenera kudya.

  • Ezekieli 4:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 Kenako ine ndinati: “Chonde Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, ine sindine woipitsidwa.+ Sindinadyepo nyama yopezeka itafa kapena nyama yochita kukhadzulidwa ndi chilombo kuyambira ndili mwana+ mpaka panopo, ndipo m’kamwa mwanga simunalowepo nyama yodetsedwa.”+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena