14 Ndikudziwa ndipo ndikukhulupirira mwa Ambuye Yesu kuti palibe chakudya chodetsedwa mwa icho chokha.+ Koma ngati munthu akuona chinachake monga chodetsedwa, kwa iyeyo ndi chodetsedwa.+
15 Zinthu zonse n’zoyera kwa anthu oyera.+ Koma kwa anthu oipitsidwa+ ndi opanda chikhulupiriro+ kulibe choyera, m’malomwake maganizo awo ndi chikumbumtima+ chawo n’zoipa.