6 Koma Timoteyo wangofika kumene kwa ife kuchokera kwa inu+ ndipo watiuza nkhani yabwino ya kukhulupirika kwanu ndi chikondi+ chanu. Akuti mukupitiriza kutikumbukira nthawi zonse, ndiponso mukulakalaka kutiona, monganso mmene ife tikulakalakiradi kukuonani.+