11 Mogwirizana ndi iyeyo tinaikidwa kukhala odzalandira cholowa,+ pakuti anatisankhiratu mwa kufuna kwake, iye amene amayendetsa zinthu zonse mogwirizana ndi chifuniro chake.+
9 Iye anatipulumutsa+ ndi kutiitana kuti tikhale oyera,+ osati chifukwa cha ntchito zathu,+ koma mwa chifuniro chake ndi kukoma mtima kwake kwakukulu. Iye anatikomera mtima m’njira imeneyi kalekalelo mwa Khristu Yesu.+