Salimo 118:22 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 22 Mwala umene omanga nyumba anaukana+Wakhala mwala wofunika kwambiri wapakona.+ Mateyu 21:42 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 42 Ndiyeno Yesu anawafunsa kuti: “Kodi simunawerenge zimene Malemba amanena zakuti, ‘Mwala umene omanga nyumba anaukana+ ndi umene wakhala mwala wapakona wofunika kwambiri.+ Umenewu wachokera kwa Yehova, ndipo ndi wodabwitsa m’maso mwathu’? 1 Petulo 2:6 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 6 Pakuti Lemba limati: “Inetu ndikuika mwala m’Ziyoni, mwala wochita kusankhidwa mwapadera, wapakona pa maziko, wamtengo wapatali, ndipo aliyense woukhulupirira sadzakhumudwa.”+
42 Ndiyeno Yesu anawafunsa kuti: “Kodi simunawerenge zimene Malemba amanena zakuti, ‘Mwala umene omanga nyumba anaukana+ ndi umene wakhala mwala wapakona wofunika kwambiri.+ Umenewu wachokera kwa Yehova, ndipo ndi wodabwitsa m’maso mwathu’?
6 Pakuti Lemba limati: “Inetu ndikuika mwala m’Ziyoni, mwala wochita kusankhidwa mwapadera, wapakona pa maziko, wamtengo wapatali, ndipo aliyense woukhulupirira sadzakhumudwa.”+