14 Chotero, popeza tili ndi mkulu wa ansembe wapamwamba, Yesu Mwana wa Mulungu,+ amene anapita kumwamba,+ tiyeni tipitirize kulengeza chikhulupiriro chathu mwa iye.+
24 Pakuti Khristu sanalowe m’malo oyera amkatikati opangidwa ndi manja a anthu,+ amene ndi chithunzi cha malo enieniwo,+ koma analowa kumwamba kwenikweniko.+ Tsopano ali kumwamba kuti aonekere pamaso pa Mulungu chifukwa cha ife.+