4 Pomalizira abale, tinakulangizani za mmene muyenera kuyendera+ ndi mmene muyenera kukondweretsera Mulungu, ndipo mukuchitadi zimenezo. Tsopano tikufuna kukudandaulirani ndi kukupemphani mādzina la Ambuye Yesu kuti mupitirize kuchita zimenezi mowonjezereka.+