15 Ndiye chofunika n’chiyani? Ndipemphere ndi mphatso ya mzimu, koma ndipempherenso ndi maganizo anga. Ndiimbe chitamando ndi mphatso ya mzimu,+ koma ndiimbenso ndi maganizo anga.+
16 Mawu a Khristu akhazikike mwa inu ndipo akupatseni nzeru zonse.+ Pitirizani kuphunzitsana+ ndi kulangizana mwa masalimo,+ nyimbo zotamanda Mulungu, ndi nyimbo zauzimu+ zogwira mtima. Pitirizani kuimbira Yehova+ m’mitima yanu.