13 Komatu anthuwo adzakondwera ndi kusangalala. Adzapha ng’ombe ndi nkhosa. Adzadya nyama ndi kumwa vinyo.+ Iwo adzati, ‘Tiyeni tidye ndi kumwa, pakuti mawa tifa.’”+
4 Anthu inu mukugona pamipando ya minyanga ya njovu+ ndi kudziwongola pamabedi, ndiponso mukudya nyama ya ana a nkhosa ndi ana amphongo onenepa a ng’ombe zanu.+