19 Mukanakhala mbali ya dziko, dziko likanakukondani monga mbali yake.+ Koma popeza simuli mbali ya dzikoli,+ koma ine ndinakusankhani kuchokera m’dziko, pa chifukwa chimenechi dziko likudana nanu.+
13 Onsewa anafa ali ndi chikhulupiriro,+ ngakhale kuti sanaone kukwaniritsidwa kwa malonjezowo.+ Koma anawaona ali patali+ ndi kuwalandira, ndipo analengeza poyera kuti iwo anali alendo ndi osakhalitsa m’dzikolo.+