12 Ngati anthu ena amagwiritsa ntchito ufulu umenewu pa inu,+ kodi ife sitili oyenera kutero kuposa amenewo? Ngakhale zili choncho, sitinagwiritse ntchito ufulu umenewo,+ koma timadzichitira tokha zinthu zonse, kuti tisapereke chododometsa chilichonse ku uthenga wabwino+ wonena za Khristu.