Chivumbulutso 3:18 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 18 Chotero, ndikukulangiza kuti ugule kwa ine golide+ woyengedwa ndi moto, kuti ukhale wolemera. Ugulenso malaya akunja oyera uvale, kuti maliseche ako asaonekere+ chifukwa ungachite manyazi. Ndiponso ugule mankhwala opaka m’maso+ ako kuti uone. Chivumbulutso 6:11 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 11 Aliyense wa iwo anapatsidwa mkanjo woyera,+ ndipo anauzidwa kuti apumulebe kanthawi pang’ono, kufikira chitakwanira chiwerengero cha akapolo anzawo, ndi abale awo amene anali pafupi kuphedwa+ monga mmene iwonso anaphedwera.
18 Chotero, ndikukulangiza kuti ugule kwa ine golide+ woyengedwa ndi moto, kuti ukhale wolemera. Ugulenso malaya akunja oyera uvale, kuti maliseche ako asaonekere+ chifukwa ungachite manyazi. Ndiponso ugule mankhwala opaka m’maso+ ako kuti uone.
11 Aliyense wa iwo anapatsidwa mkanjo woyera,+ ndipo anauzidwa kuti apumulebe kanthawi pang’ono, kufikira chitakwanira chiwerengero cha akapolo anzawo, ndi abale awo amene anali pafupi kuphedwa+ monga mmene iwonso anaphedwera.