2 Munali kuyenda m’zimenezo mogwirizana ndi nthawi*+ za m’dzikoli, momveranso wolamulira+ wa mpweya umene umalamulira zochita za anthu. Mpweya umenewu, kapena kuti kaganizidwe kameneka,+ tsopano kakugwira ntchito mwa ana a kusamvera.+
12 chifukwa sitikulimbana+ ndi anthu athupi la magazi ndi nyama ayi, koma ndi maboma,+ maulamuliro,+ olamulira dziko+ a mdimawu, ndi makamu a mizimu yoipa+ m’malo akumwamba.