Zefaniya
1 M’masiku a Yosiya+ mwana wa Amoni+ mfumu ya Yuda, Yehova analankhula kudzera mwa Zefaniya mwana wa Kusa, mwana wa Gedaliya, mwana wa Amariya, mwana wa Hezekiya. Iye anati:
2 “Ine ndidzafafaniza chilichonse chimene chili panthaka,” watero Yehova.+
3 “Ndidzafafaniza anthu ndi nyama.+ Ndidzafafaniza zolengedwa zouluka m’mlengalenga, nsomba za m’nyanja,+ zokhumudwitsa pamodzi ndi anthu oipa,+ ndipo ndidzawononga anthu onse ndi kuwachotsa panthaka,”+ watero Yehova. 4 “Ndidzatambasula dzanja langa ndi kuwononga Yuda pamodzi ndi anthu onse okhala mu Yerusalemu.+ Ndidzawononga anthu onse otsala amene amapembedza Baala+ ndi kuwachotsa pamalo ano. Ndidzafafanizanso dzina la ansembe a mulungu wachilendo pamodzi ndi ansembe ena.+ 5 Ndidzafafaniza anthu amene akugwadira khamu la zinthu zakuthambo pamadenga* a nyumba zawo,+ ndiponso amene akugwada ndi kulumbira+ kuti adzakhala okhulupirika kwa Yehova+ koma amakhalanso akulumbira m’dzina la Malikamu.+ 6 Ndidzafafaniza amene akusiya kutsatira Yehova,+ amene sanayesetse kuyandikira Yehova ndi amene sanafunsire kwa iye.”+
7 Khalani chete pamaso pa Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa,+ pakuti tsiku la Yehova lili pafupi,+ ndipo Yehova wakonza nsembe+ moti wakonzekeretsa*+ anthu amene wawaitana.
8 “Ndiyeno pa tsiku limene Yehova adzapereka nsembe, ine ndidzalanga akalonga, ana a mfumu+ ndi onse ovala zovala zachilendo.+ 9 Pa tsiku limenelo, ndidzalanga aliyense amene ali pafupi ndi mpando wachifumu, anthu amene adzaza nyumba za ambuye awo ndi chiwawa ndiponso chinyengo.+ 10 Pa tsiku limenelo,” watero Yehova, “ku Chipata cha Nsomba+ kudzamveka phokoso la kulira ndipo kuchigawo chatsopano cha mzinda+ kudzamveka phokoso la kulira mokweza. Kumapiri+ kudzamveka phokoso la chiwonongeko chachikulu. 11 Lirani mofuula+ anthu inu okhala ku Makitesi, pakuti amalonda onse awonongedwa+ ndipo onse amene amayeza siliva pasikelo aphedwa.
12 “Pa nthawi imeneyo ndidzafufuza ndi nyale mu Yerusalemu mosamala kwambiri,+ ndipo ndidzalanga anthu amene akukhala mosatekeseka ngati vinyo amene nsenga zake zakhazikika pansi.+ M’mitima yawo, anthu amenewa akunena kuti, ‘Yehova sadzachita zabwino kapena kuchita zoipa.’+ 13 Chuma chawo chidzafunkhidwa ndipo nyumba zawo zidzakhala bwinja.+ Iwo adzamanga nyumba, koma sadzakhalamo.+ Iwo adzalima minda ya mpesa koma sadzamwa vinyo wochokera mmenemo.+
14 “Tsiku lalikulu+ la Yehova lili pafupi.+ Lili pafupi ndipo likubwera mofulumira kwambiri.+ Mkokomo wa tsiku la Yehova ukubwera ndi zowawa.+ Pa tsiku limenelo mwamuna wamphamvu adzalira.+ 15 Tsiku limenelo ndi tsiku lamkwiyo, tsiku lansautso ndi zowawa,+ tsiku la mphepo yamkuntho ndi losakaza, tsiku lamdima wochititsa mantha,+ tsiku lamitambo yakuda ndi lamdima wandiweyani. 16 Pa tsiku limenelo, lipenga la nyanga ya nkhosa ndiponso chizindikiro chochenjeza zidzalira+ pochenjeza mizinda yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri, komanso nsanja zazitali kwambiri za m’makona.+ 17 Pamenepo ndidzasautsa mtundu wa anthu moti adzayenda ngati anthu akhungu+ chifukwa chakuti iwo achimwira Yehova.+ Magazi awo adzakhuthulidwa pansi ngati fumbi,+ ndipo matumbo awo adzakhuthulidwa pansi ngati ndowe.+ 18 Siliva kapena golide wawo sadzawapulumutsa pa tsiku la mkwiyo wa Yehova.+ Moto wa mkwiyo wake udzanyeketsa dziko lonse lapansi,+ chifukwa iye adzafafaniza anthu onse okhala padziko lapansi.”+