Masalimo
Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimbo ya Davide.
13 Kodi mudzandiiwala kufikira liti, inu Yehova?+ Mpaka muyaya?+
Mudzandibisira nkhope yanu kufikira liti?+
2 Kodi ndidzalimbana ndi masautso anga kufikira liti?
Kodi masiku a moyo wanga adzakhala odzaza ndi chisoni kufikira liti?
Kodi mdani wanga adzadzikweza pamaso panga kufikira liti?+
3 Ndiyang’aneni. Ndiyankheni, inu Yehova Mulungu wanga.
Walitsani maso anga+ kuti ndisagone mu imfa.+
4 Chitani zimenezi kuti mdani wanga asanene kuti: “Ndamugonjetsa!”
Kutinso adani anga asakondwere chifukwa chakuti ine ndadzandira.+
5 Koma ine ndakhulupirira kukoma mtima kwanu kosatha.+
Mtima wanga ukondwere chifukwa cha chipulumutso chanu.+
6 Ndidzaimbira Yehova chifukwa wandifupa ndi zinthu zabwino.+