Masalimo
Nyimbo ya Davide.
143 Inu Yehova, imvani pemphero langa.+
Tcherani khutu pamene ndikuchonderera.+
Ndiyankheni mogwirizana ndi kukhulupirika kwanu ndi chilungamo chanu.+
2 Musandiimbe mlandu ine mtumiki wanu,+
Pakuti palibe aliyense wamoyo amene angakhale wolungama pamaso panu.+
3 Mdani akufunafuna moyo wanga,+
Iye waupondaponda pafumbi.+
Wandichititsa kukhala m’malo a mdima ngati anthu amene anafa kalekale.+
Ndasinkhasinkha zochita zanu zonse,+
Ndipo ndakhala ndikuganizira ntchito ya manja anu ndi mtima wonse.+
6 Ine ndikupemphera nditakweza manja anga kwa inu.+
Moyo wanga uli ngati dziko louma limene likulakalaka kuti muthetse ludzu lake.+ [Seʹlah.]
7 Fulumirani, ndiyankheni inu Yehova.+
Mphamvu zanga zatha.+
Musandibisire nkhope yanu,+
Chifukwa mukatero ndikhala ngati anthu amene akutsikira kudzenje la manda.+
8 M’mawa ndichititseni kumva za kukoma mtima kwanu kosatha,+
Pakuti ndimadalira inu.+
Ndidziwitseni njira imene ndiyenera kuyendamo,+
Pakuti ndapereka moyo wanga kwa inu.+
10 Ndiphunzitseni kuchita chifuniro chanu,+
Pakuti inu ndinu Mulungu wanga.+
Mzimu wanu ndi wabwino.+
Unditsogolere m’dziko la olungama.+