Masalimo
Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimbo ya Davide.
3 Akumbukire nsembe zanu zonse zimene munapereka monga mphatso.+
Alandire mafuta a nsembe zanu zopsereza.+ [Seʹlah.]
5 Tidzafuula mokondwera chifukwa cha chipulumutso chanu,+
Tidzakweza mbendera zathu m’dzina la Mulungu wathu.+
Yehova akwaniritse zopempha zanu zonse.+
6 Tsopano ndadziwa kuti Yehova amapulumutsa wodzozedwa wake.+
Amamuyankha kuchokera kumwamba kwake koyera,+
Amamupulumutsa ndi dzanja lake lamanja lamphamvu zopulumutsa.+