Masalimo
104 Tamanda Yehova, iwe moyo wanga.+
Inu Yehova Mulungu wanga, mwasonyeza kuti ndinu wamkulu koposa.+
Mwadziveka ulemu ndi ulemerero.+
2 Mwadzifunditsa kuwala ngati chofunda,+
Mwatambasula kumwamba ngati nsalu ya chihema.+
3 Inu munamanga zipinda za m’mwamba pamadzi pogwiritsa ntchito mitanda,+
Munapanga mitambo kukhala galeta lanu,+
Mumayenda pamapiko a mphepo.+
4 Inu mumapanga angelo anu kukhala mizimu,+
Ndipo atumiki anu kukhala moto wonyeketsa.+
7 Chifukwa cha kudzudzula kwanu, madziwo anayamba kuthawa.+
Atamva mabingu anu anayamba kuthamanga mopanikizika kwambiri,
8 Kupita kumalo amene munawakonzera.
Mapiri anakwera,+
Zigwa zinatsika.
11 Akasupewo amapereka madzi kwa zilombo zonse zakutchire.+
Nthawi zonse mbidzi+ zimapha ludzu lawo mmenemo.
12 Zolengedwa zouluka m’mlengalenga zimamanga zisa zawo pafupi ndi akasupewo,+
Ndipo zimalira m’mitengo ya masamba ambiri obiriwira.+
13 Mulungu amathirira mapiri kuchokera m’zipinda zake za m’mwamba.+
Dziko lapansi ladzaza ndi zipatso za ntchito yake.+
14 Amameretsa msipu kuti nyama zidye,+
Ndipo amameretsa mbewu kuti anthu agwiritse ntchito.+
Amachita zimenezi kuti chakudya chituluke m’nthaka,+
15 Komanso kuti mutuluke vinyo amene amasangalatsa mtima wa munthu.+
Amachita zonsezi kuti nkhope ya munthu isalale ndi mafuta,+
Komanso kuti apereke chakudya chimene chimakhutiritsa mtima wa munthu.+
16 Mitengo ya Yehova imathiriridwa bwino,
Mikungudza ya ku Lebanoni imene iye anabzala.+
17 Mbalame zimamanga zisa zawo mmenemo.+
Dokowe nyumba yake ndiyo mitengo ya mlombwa.+
19 Wapanga mwezi kuti uzisonyeza nthawi yoikidwiratu.+
Dzuwa nalo limadziwa bwino kumene limalowera.+
24 Ntchito zanu ndi zochuluka, inu Yehova!+
Zonsezo munazipanga mwanzeru zanu.+
Dziko lapansi ladzaza ndi zinthu zimene munapanga.+
25 M’nyanja yakuya iyi ndiponso yotambalala,+
Muli zinthu zoyenda zosawerengeka,+
Muli zamoyo zazikulu ndi zazing’ono zomwe.+
29 Mukaphimba nkhope yanu, zimasokonezeka.+
Mukachotsa mzimu wawo, zimafa,+
Ndipo zimabwerera kufumbi.+