Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimbo ndi Salimo la ana a Kora.
47 Ombani m’manja anthu nonsenu.+
Fuulirani Mulungu mokondwera chifukwa chakuti wapambana.+
2 Pakuti Yehova, Wam’mwambamwamba, ndi wochititsa mantha,+
Ndiye Mfumu yaikulu padziko lonse lapansi.+
3 Iye adzagonjetsa mitundu ya anthu ndi kuiika pansi pathu.+
Adzagonjetsa anthu a mitundu ina ndi kuwaika pansi pa mapazi athu.+
4 Adzatisankhira cholowa,+
Chimene Yakobo, amene amamukonda, anakondwera nacho.+ [Seʹlah.]
5 Mulungu wakwera kumalo ake, anthu akufuula mokondwera,+
Yehova wakwera kumalo ake, anthu akuliza lipenga la nyanga ya nkhosa.+
6 Imbani nyimbo zotamanda Mulungu, imbani nyimbo zotamanda.+
Imbani nyimbo zotamanda Mfumu yathu, imbani nyimbo zotamanda.
7 Pakuti Mulungu ndi Mfumu ya dziko lonse lapansi.+
Imbani nyimbo zotamanda ndi kuchita zinthu mozindikira.+
8 Mulungu wakhala mfumu ya mitundu ya anthu.+
Mulungu wakhala pampando wake wachifumu wopatulika.+
9 Atsogoleri a mitundu ya anthu asonkhana.+
Asonkhana pamodzi ndi anthu a Mulungu wa Abulahamu.+
Pakuti anthu onse omwe ali ngati zishango za dziko lapansi ndi a Mulungu.+
Iye wakwera pamalo okwezeka kwambiri.+