Zekariya
9 Uthenga+ wokhudza dziko la Hadiraki:
“Awa ndi mawu a Yehova oweruza dziko la Hadiraki, ndipo akuweruzanso Damasiko.+ Pakuti maso a Yehova akuyang’ana anthu+ komanso mafuko onse a Isiraeli. 2 Mawu amenewa akuweruzanso Hamati+ amene anachita naye malire. Komanso akuweruza Turo+ ndi Sidoni+ chifukwa ali ndi nzeru zambiri.+ 3 Turo anamanga chiunda chomenyerapo nkhondo.* Anadziunjikira siliva wochuluka ngati dothi ndiponso golide wochuluka ngati matope a m’misewu.+ 4 Yehova adzamulanda chuma chake ndipo gulu lake lankhondo adzaliphera m’nyanja.+ Koma iye adzatenthedwa ndi moto.+ 5 Asikeloni adzaona zimenezi ndipo adzachita mantha. Gaza adzamva ululu waukulu. Izi zidzachitikiranso Ekironi+ chifukwa chakuti amene anali kumudalira+ adzachita manyazi. Ku Gaza sikudzakhalanso mfumu ndipo m’dziko la Asikeloni simudzakhalanso anthu.+ 6 Mwana wochokera mu mtundu wina wa anthu+ adzakhala mu Asidodi,+ ndipo ine ndidzathetsa kunyada kwa Afilisiti.+ 7 Ndidzachotsa zinthu zake zamagazi m’kamwa mwake ndipo ndidzachotsa chakudya chake chonyansa pakati pa mano ake.+ Aliyense amene adzatsale adzakhala wa Mulungu wathu. Wotsalayo adzakhala ngati mfumu+ mu Yuda,+ ndipo Ekironi adzakhala ngati Myebusi.+ 8 Ndidzamanga msasa kunja kwa nyumba yanga kuti ndizidzailondera,+ moti sipadzakhalanso munthu wolowa kapena kutuluka. Kapitawo sadzadutsanso pakati pawo+ pakuti ine ndaona ndi maso anga zimene zinawachitikira.+
9 “Iwe mwana wamkazi wa Ziyoni sangalala kwambiri.+ Fuula mokondwera+ iwe mwana wamkazi wa Yerusalemu. Taona, mfumu yako+ ikubwera kwa iwe.+ Mfumuyo ndi yolungama ndipo yapambana.+ Iyo ndi yodzichepetsa+ ndipo ikubwera itakwera bulu. Ikubwera itakwera nyama yokhwima, imene ndi mwana wamphongo wa bulu.+ 10 Ndidzawononga magaleta ankhondo mu Efuraimu ndiponso mahatchi mu Yerusalemu.+ Mauta omenyera nkhondo+ adzathyoledwa. Mfumuyo idzalankhula mawu amtendere kwa anthu a mitundu ina.+ Ulamuliro wake udzayambira kunyanja mpaka kukafika kunyanja. Ndiponso udzachokera ku Mtsinje* mpaka kumalekezero a dziko lapansi.+
11 “Koma mkazi iwe, chifukwa cha magazi a pangano limene unapangana ndi ine,+ ndidzatulutsa akaidi ako+ m’dzenje lopanda madzi.
12 “Inu akaidi amene muli ndi chiyembekezo,+ bwererani kumalo a chitetezo champhamvu.+
“Komanso, ine lero ndikunena kuti, ‘Mkazi iwe, ndidzakupatsa magawo awiri a madalitso.+ 13 Yuda ndidzamupinda kuti akhale uta wanga. Efuraimu ndidzamuika pa uta umenewo ngati muvi. Iwe Ziyoni, ine ndidzadzutsa ana ako+ kuti aukire ana a Girisi.+ Ndipo ndidzakusandutsa lupanga la munthu wamphamvu.’+ 14 Zidzakhala zoonekeratu kuti Yehova ali ndi anthu ake,+ ndipo muvi wake udzathamanga ngati mphezi.+ Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa adzaliza lipenga lanyanga ya nkhosa,+ ndipo adzapita ndi mphepo yamkuntho ya kum’mwera.+ 15 Yehova wa makamu adzatchinjiriza anthu ake. Adani awo adzawalasa ndi miyala yoponya ndi gulaye* koma iwo adzagonjetsa adaniwo.+ Iwo adzasangalala ndipo adzafuula ngati amwa vinyo.+ Adzadzazidwa ngati mbale zolowa ndiponso ngati mmene magazi amadzazira m’makona a guwa lansembe.+
16 “Pa tsiku limenelo, Yehova Mulungu adzapulumutsa nkhosa zake,+ zimene ndi anthu ake.+ Pakuti iwo adzakhala ngati miyala yonyezimira ya pachisoti chachifumu m’dziko lake.+ 17 Ubwino wake ndi waukulu kwambiri+ ndiponso iye ndi wooneka bwino kwambiri.+ Tirigu adzapatsa mphamvu anyamata ndipo vinyo watsopano adzapatsa mphamvu anamwali.”+