Masalimo
Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimbo ndi Salimo la Davide.
139 Inu Yehova, mwandifufuza ndipo mukundidziwa.+
3 Mumandidziwa bwino pamene ndikuyenda komanso pamene ndikugona,+
Ndipo njira zanga zonse mukuzidziwa bwino.+
5 Mwandizungulira,
Ndipo mwaika dzanja lanu pa ine.
6 Kwa ine ndi zovuta kwambiri kuti ndidziwe zinthu zonsezi.+
Ndi zapamwamba kwambiri moti sindingathe kuzifikira.+
8 Ngati ndingakwere kumwamba, inu mudzakhala komweko.+
Ndipo ngati ndingayale bedi langa ku Manda, taonani! inunso mudzakhala komweko.+
9 Ngati ndingakwere pamapiko+ a m’bandakucha,
Kuti ndikakhale m’nyanja ya kutali kwambiri,+
10 Kumenekonso dzanja lanu lidzanditsogolera,+
Dzanja lanu lamanja lidzandigwira.+
11 Ngati ndinganene kuti: “Ndithudi mdima undipeze mofulumira!”+
Pamenepo mdima udzasanduka kuwala pa ine.+
12 Ndipo mdimawo sudzakhala mdima wandiweyani kwa inu,+
Koma usiku udzakuwalirani ngati masana.+
Mdima udzangokhala ngati kuwala.+
14 Ndidzakutamandani chifukwa munandipanga modabwitsa ndipo zimenezi zimandichititsa mantha.+
Ntchito zanu ndi zodabwitsa,+
Ndipo ine ndimadziwa bwino zimenezi.+
15 Mafupa anga sanali obisika kwa inu+
Pamene munali kundipanga m’malo obisika,+
Pamene munali kundiwomba ngati nsalu m’malo apansi kwambiri+ padziko lapansi.
16 Maso anu anandiona pamene ndinali mluza,+
Ndipo ziwalo zanga zonse zinalembedwa m’buku lanu.
M’bukumo munalembamo za masiku amene zinapangidwa+
Koma panalibe ngakhale chiwalo chimodzi chimene chinali chitapangidwa.
18 Nditati ndiyese kuwawerenga, angakhale ochuluka kwambiri kuposa mchenga.+
Podzuka ndingakhale ndikuwawerengabe.+
19 Inu Mulungu, zikanakhala bwino mukanapha woipa.+
Pamenepo anthu amene ali ndi mlandu wa magazi+ akanandichokera,