Masalimo
Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimbo ya Davide.
41 Wodala ndi munthu amene amachita zinthu moganizira munthu wonyozeka.+
Pa tsiku la tsoka, Yehova adzamupulumutsa.+
2 Yehova adzamuteteza ndi kumusunga ali wamoyo.+
Adzatchedwa wodala padziko lapansi.+
Ndipo Mulungu sangamupereke kwa adani ake.+
3 Yehova adzachirikiza wonyozekayo pamene akudwala pabedi lake.+
Mudzamusamalira bwino kwambiri pamene akudwala.+
5 Adani anga amanena zoipa zokhazokha za ine kuti:+
“Kodi ameneyu afa liti kuti dzina lake lifafanizike?”
6 Wina akabwera kudzandiona, amalankhula zabodza kuchokera mumtima mwake.+
Amasonkhanitsa nkhani zoipa.
Akatero amachoka, ndipo kunjako amauza ena zabodza zokhudza ine.+
7 Mogwirizana, onse amene amadana nane amanong’onezana kuti andiukire.+
Amandikonzera chiwembu kuti andichitire zinthu zoipa. Iwo amati:+
9 Koma munthu amene ndinali kukhala naye mwamtendere, amene ndinali kumukhulupirira,+
Munthu amene anali kudya chakudya changa,+ wakweza chidendene chake kundiukira.+
11 Mukatero ndidziwa kuti mwasangalala nane,
Chifukwa mdani wanga sadzafuula mosangalala kuti wandipambana.+