Masalimo
Weruzani mlandu wanga+ motsutsana ndi mtundu wosakhulupirika.
Ndipulumutseni kwa munthu wachinyengo ndi wochita zosalungama.+
2 Pakuti inu ndinu Mulungu wanga, ndinu malo anga achitetezo.+
N’chifukwa chiyani mwanditaya?
Ndikuyenderanji wachisoni chifukwa choponderezedwa ndi mdani wanga?+
3 Tumizani kuwala kwanu ndi choonadi chanu.+
Zimenezi zinditsogolere.+
Zindifikitse kuphiri lanu lopatulika ndi kuchihema chanu chachikulu.+