Masalimo
Kwa wotsogolera nyimbo pa Gititi.*+ Nyimbo ndi Salimo la ana a Kora.
2 Ndimalakalaka mabwalo a Yehova ndipo ndafookeratu chifukwa cholakalaka mabwalowo.+
Mtima wanga ndi thupi langa zikufuula mosangalala kwa Mulungu wamoyo.+
3 Inu Yehova wa makamu, Mfumu yanga ndi Mulungu wanga,
Ngakhale mbalame zapeza malo okhala pafupi ndi guwa lanu lansembe lalikulu.
Namzeze* wadzimangira chisa chake pamenepo,
Ndi kuikamo ana ake!
5 Odala ndi anthu amene amapeza mphamvu kuchokera kwa inu,+
Amene mtima wawo umalakalaka misewu yaikulu yopita kunyumba yanu.+
6 Poyenda m’chigwa chouma mmene muli zitsamba za baka,*+
Amasandutsa chigwacho kukhala choyenda madzi ochokera pakasupe,
Mlangizi wafunda mawu otamanda.+
7 Mphamvu zawo zidzapitiriza kuwonjezeka pamene akuyenda.+
Aliyense wa iwo amaonekera kwa Mulungu mu Ziyoni.+
8 Yehova Mulungu wa makamu, imvani pemphero langa,+
Tcherani khutu, inu Mulungu wa Yakobo.+ [Seʹlah.]
10 Pakuti kukhala tsiku limodzi m’mabwalo anu n’kwabwino kuposa kukhala masiku 1,000 kwina.+
Ndasankha kuima pakhomo la nyumba ya Mulungu wanga+
Kuposa kukhala m’mahema a anthu oipa.+
11 Pakuti Yehova Mulungu ndi dzuwa+ ndiponso chishango.+
Iye amatikomera mtima ndi kutipatsa ulemerero.+
Yehova samana anthu oyenda mosalakwa chinthu chilichonse chabwino.+
12 Inu Yehova wa makamu, wodala ndi munthu amene amakhulupirira inu.+