Genesis
25 Tsopano Abulahamu anatenganso mkazi wina, dzina lake Ketura.+ 2 M’kupita kwa nthawi, mkaziyo anamuberekera Zimirani, Yokesani, Medani, Midiyani,+ Isibaki ndi Shuwa.+
3 Yokesani anabereka Sheba+ ndi Dedani.+
Ana a Dedani anali Asurimu, Letusimu ndi Leumimu.
4 Ana a Midiyani anali Efa,+ Eferi, Hanoki, Abida ndi Elida.+
Onsewa anali ana aamuna a Ketura.
5 Pambuyo pake, Abulahamu anapatsa Isaki zonse zimene anali nazo.+ 6 Koma ana a adzakazi amene Abulahamu anali nawo, anawapatsa mphatso.+ Kenako, iye adakali ndi moyo, anatumiza anawo+ Kum’mawa,+ kutali ndi mwana wake Isaki. 7 Masiku onse a moyo wa Abulahamu anali zaka 175. 8 Kenako, Abulahamu anamwalira ali wokalamba, atakhala ndi moyo wabwino, wautali ndi wokhutira, ndipo anaikidwa m’manda n’kugona ndi makolo ake.+ 9 Chotero ana ake, Isaki ndi Isimaeli, anamuika iye m’manda. Anamuika m’phanga la Makipela, kumalo a Efuroni mwana wa Zohari Mheti, moyang’anana ndi Mamure.+ 10 Malo amenewa ndi omwe Abulahamu anagula kwa ana a Heti. Abulahamu anaikidwa kumeneko, komanso Sara mkazi wake.+ 11 Abulahamu atamwalira, Mulungu anapitiriza kudalitsa Isaki mwana wake.+ Isakiyo anali kukhala pafupi ndi Beere-lahai-roi.+
12 Tsopano nayi mbiri ya Isimaeli+ mwana wa Abulahamu, amene Hagara Mwiguputo, kapolo wa Sara anaberekera Abulahamu.+
13 Awa ndiwo mayina a ana a Isimaeli, amene kunachokera mabanja awo: Nebayoti,+ mwana woyamba wa Isimaeli, Kedara,+ Adibeele, Mibisamu,+ 14 Misima, Duma, Maasa, 15 Hadadi,+ Tema,+ Yeturi, Nafisi ndi Kedema.+ 16 Amenewa ndiwo ana a Isimaeli, potsata mayina awo, malinga ndi midzi yawo ndi misasa yawo yotchinga ndi mipanda.+ Anali atsogoleri okwanira 12 malinga ndi mafuko awo.+ 17 Zaka zonse zimene Isimaeli anakhala ndi moyo zinali 137. Kenako anamwalira, ndipo anaikidwa m’manda n’kugona ndi makolo ake.+ 18 Iwo anakhala m’mahema kuyambira ku Havila+ pafupi ndi Shura+ moyang’anana ndi Iguputo, mpaka ku Asuri. Anakhala pafupi ndi abale awo onse.+
19 Tsopano nayi mbiri ya Isaki mwana wa Abulahamu.+
Abulahamu anabereka Isaki. 20 Isaki anali ndi zaka 40 pamene anakwatira Rabeka, mwana wa Betuele,+ Msiriya+ wa ku Padana-ramu, mlongo wake wa Labani, Msiriya. 21 Isaki anali kupembedzera Yehova mosalekeza, makamaka chifukwa cha mkazi wake,+ popeza iye anali wosabereka.+ Yehova anamva kupembedzera kwake,+ ndipo Rabeka mkazi wakeyo anakhala ndi pakati. 22 Ndiyeno ana amene anali m’mimba mwake anayamba kulimbana,+ moti iye anati: “Ngati umu ndi mmene ndivutikire, ndiye ndi bwino ndingofa.” Atatero anapita kukafunsira kwa Yehova.+ 23 Yehova anamuyankha kuti: “M’mimba mwako+ muli mitundu iwiri ya anthu, ndipo mitundu iwiri imene idzatuluka m’mimba mwakoyo idzakhala yosiyana.+ Mtundu wina udzakhala wamphamvu kuposa mtundu winawo,+ ndipo wamkulu adzatumikira wamng’ono.”+
24 Potsirizira pake, masiku oti Rabeka abereke anakwana, ndipo m’mimba mwake munali mapasa.+ 25 Woyamba kubadwa anali wofiira, ndipo thupi lake lonse linali ngati wavala chovala chaubweya.+ Ndiye chifukwa chake anamutcha dzina lakuti Esau.*+ 26 Pambuyo pa iyeyu, panabadwa m’bale wake, dzanja lake litagwira chidendene cha Esau,+ choncho Isaki anapatsa mwanayo dzina lakuti Yakobo.+ Pamene Rabeka amabereka anawa n’kuti Isaki ali ndi zaka 60.
27 Anyamatawa anakula, ndipo Esau anakhala munthu wodziwa kusaka,+ munthu wokonda kuyenda m’tchire. Koma Yakobo anali kukhala nthawi yambiri m’mahema.+ Iye anali munthu wosalakwa.+ 28 Isaki anali kukonda kwambiri Esau chifukwa anali kum’phera nyama, koma Rabeka anali kukonda kwambiri Yakobo.+ 29 Tsiku lina Yakobo akuphika mphodza, Esau anafika kuchokera kutchire, ndipo anali atatopa. 30 Ndiyeno Esau anapempha Yakobo kuti: “Chonde, fulumira ndipatseko chakudya chofiiracho pang’ono, icho chofiiracho! Ndatopatu ine!” Ndiye chifukwa chake anatchedwa Edomu.*+ 31 Pamenepo Yakobo anayankha kuti: “Choyamba, undigulitse ukulu wako monga woyamba kubadwa.”+ 32 Esau anati: “Ine pano ndifa ndithu ndi njala, ndiye ukuluwo uli ndi phindu lanji kwa ine?” 33 Ndiyeno Yakobo anati: “Choyamba lumbira kwa ine!”+ Ndipo iye analumbiradi kwa Yakobo, n’kugulitsa kwa iye ukulu wake monga woyamba kubadwa.+ 34 Pamenepo Yakobo anapatsa Esau mkate ndi mphodza, ndipo iye anadya n’kumwa.+ Kenako, ananyamuka n’kumapita. Umu ndi mmene Esau ananyozera ukulu wake.+