97 Yehova wakhala mfumu!+ Dziko lapansi likondwere,+
Ndipo zilumba zambiri zisangalale.+
2 Mitambo ndi mdima wandiweyani zamuzungulira.+
Chilungamo ndi chiweruzo ndizo malo okhazikika a mpando wake wachifumu.+
3 Patsogolo pake pakuyaka moto,+
Ndipo ukupsereza adani ake onse omuzungulira.+
4 Mphezi zake zinawalitsa dziko lapansi.+
Dziko linaona ndipo linachita mantha kwambiri.+
5 Mapiri anasungunuka ngati phula chifukwa cha Yehova,+
Chifukwa cha Ambuye wa dziko lonse lapansi.+
6 Kumwamba kwalengeza za chilungamo chake,+
Ndipo mitundu yonse ya anthu yaona ulemerero wake.+
7 Onse amene akupembedza chifaniziro chilichonse achite manyazi.+
Amene amadzitama chifukwa cha milungu yopanda pake achite manyazi.+
Muweramireni, inu milungu yonse.+
8 Ziyoni anamva ndipo anayamba kusangalala,+
Midzi yozungulira Yuda inayamba kukondwera+
Chifukwa cha zigamulo zanu, inu Yehova.+
9 Pakuti inu Yehova, ndinu Wam’mwambamwamba wolamulira dziko lonse lapansi.+
Mwakwera pamwamba kwambiri kuposa milungu ina yonse.+
10 Inu okonda Yehova+ danani nacho choipa.+
Iye amateteza moyo wa anthu ake okhulupirika.+
Amawalanditsa m’manja mwa anthu oipa.+
11 Kuwala kwaunikira wolungama,+
Ndipo anthu owongoka mtima akusangalala.+
12 Sangalalani chifukwa cha Yehova, anthu olungama inu,+
Ndipo yamikirani dzina lake loyera.+