116 Mtima wanga ndi wodzaza ndi chikondi, chifukwa Yehova amamva+
Mawu anga ndi madandaulo anga.+
2 Pakuti watchera khutu lake kwa ine,+
Ndipo ndidzaitanira pa iye masiku onse a moyo wanga.+
3 Zingwe za imfa zinandizungulira+
Ndipo ndinasautsika ngati kuti ndili m’Manda.+
Ndinapitiriza kusautsika ndi kukhala wachisoni,+
4 Koma ndinaitana pa dzina la Yehova kuti:+
“Inu Yehova, pulumutsani moyo wanga!”+
5 Yehova ndi wachisomo ndi wolungama.+
Mulungu wathu amasonyeza chifundo.+
6 Yehova amateteza anthu osadziwa zambiri.+
Ndinali wosautsika koma iye anandipulumutsa.+
7 Iwe moyo wanga, bwerera kumalo ako ampumulo,+
Pakuti Yehova wakuchitira zinthu zabwino.+
8 Pakuti inu mwapulumutsa moyo wanga ku imfa,+
Mwateteza maso anga kuti asakhetse misozi ndiponso phazi langa kuti lisapunthwe.+
9 Ndidzayenda+ pamaso pa Yehova m’dziko la anthu amoyo.+
10 Ndinali ndi chikhulupiriro,+ n’chifukwa chake ndinalankhula.+
Ndinali kusautsika kwambiri.
11 Pamene ndinapanikizika ndinati:+
“Munthu aliyense ndi wabodza.”+
12 Yehova ndidzamubwezera chiyani+
Pa zabwino zonse zimene wandichitira?+
13 Ndidzamwa za m’kapu yachipulumutso chachikulu,+
Ndipo ndidzaitana pa dzina la Yehova.+
14 Ndidzakwaniritsa malonjezo anga kwa Yehova,+
Pamaso pa anthu ake onse.
15 M’maso mwa Yehova
Imfa ya anthu ake okhulupirika ndi nkhani yaikulu.+
16 Inu Yehova,+
Inetu ndine mtumiki wanu.+
Ndine mtumiki wanu, mwana wa kapolo wanu wamkazi.+
Mwamasula zingwe zimene anandimanga nazo.+
17 Ndidzapereka nsembe zoyamikira kwa inu,+
Ndipo ndidzaitana pa dzina la Yehova.+
18 Ndidzakwaniritsa malonjezo anga kwa Yehova,+
Ndidzawakwaniritsa pamaso pa anthu ake onse,+
19 M’mabwalo a nyumba ya Yehova,+
Pakati pa iwe Yerusalemu.+
Tamandani Ya, anthu inu!+