Masalimo
Kwa wotsogolera nyimbo pa Yedutuni.* Nyimbo ya Davide.
2 Iye ndiye thanthwe langa ndi chipulumutso changa, malo anga okwezeka ndiponso achitetezo.+
Sindidzagwedezeka kwambiri.+
3 Kodi mudzayesayesa kufikira liti kuti muphe munthu amene mumadana naye?+
Nonsenu muli ngati khoma lopendekeka, khoma lamiyala limene akulikankha kuti ligwe.+
4 Iwo amapatsa munthu malangizo kuti amukope ndi kumutsitsa pamalo ake aulemu.+
Bodza limawasangalatsa.+
Iwo amadalitsa ndi pakamwa pawo, koma mumtima mwawo amatemberera.+ [Seʹlah.]
5 Ndithudi, yembekezera Mulungu modekha, iwe moyo wanga,+
Chifukwa chiyembekezo changa chichokera kwa iye.+
6 Ndithudi, iye ndi thanthwe langa ndi chipulumutso changa, malo anga okwezeka ndiponso achitetezo.+
Sindidzagwedezeka.+
7 Chipulumutso ndi ulemerero wanga zili mwa Mulungu.+
Iye ndi thanthwe langa lolimba ndi malo anga othawirako.+
8 Mukhulupirireni nthawi zonse, anthu inu.+
Mukhuthulireni za mumtima mwanu.+
Mulungu ndiye pothawirapo pathu.+ [Seʹlah.]
9 Ndithudi, ana a anthu ochokera kufumbi ali ngati mpweya,+
Ana a anthu ndi malo othawirako achinyengo.+
Onse pamodzi akaikidwa pasikelo ndi opepuka kuposa mpweya.+