Masalimo
Salimo la Davide.
29 M’patseni Yehova, inu amphamvu,*
M’patseni Yehova ulemerero ndipo vomerezani kuti iye ndi wamphamvu.+
2 M’patseni Yehova ulemerero woyenera dzina lake.+
Weramirani Yehova mutavala zovala zopatulika zokongola.+
3 Liwu la Yehova lili pamwamba pa madzi,*+
Liwu la Mulungu waulemerero+ lagunda ngati bingu.+
Yehova ali pamwamba pa madzi ambiri.+
5 Liwu la Yehova likuthyola mitengo ya mkungudza,
Yehova akuthyolathyola mitengo ya mkungudza ya ku Lebanoni.+
6 Iye akuichititsa kudumphadumpha ngati mwana wa ng’ombe,+
Lebanoni ndi Sirioni+ akudumphadumpha ngati ana a ng’ombe zakutchire.
7 Liwu la Yehova likutulutsa malawi a moto.+
8 Liwu la Yehova likuchititsa chipululu kuphiriphitha,+
Yehova akuchititsa chipululu cha Kadesi+ kuphiriphitha.
9 Liwu la Yehova likuchititsa mbawala zazikazi kuphiriphitha ndi ululu wa pobereka,+
Ndipo likufafaniza nkhalango.+
M’kachisi wake aliyense akunena kuti: “Ulemerero ndi wa Mulungu!”+