Masalimo
Kwa wotsogolera nyimbo. Salimo la Davide.
11 Ine ndathawira kwa Yehova.+
Kodi mulibe mantha? Mukundiuza kuti:
“Thawirani kumapiri anu ngati mbalame!+
Akonzekeretsa mivi yawo kuti aiponye ndi uta,
Kuti alase anthu owongoka mtima kuchokera pamalo amdima.+
4 Yehova ali m’kachisi wake wopatulika.+
Yehova, mpando wake wachifumu uli kumwamba.+
Maso ake amaona, maso ake owala amasanthula+ ana a anthu.
5 Yehova amasanthula anthu olungama ndi oipa omwe,+
Ndipo Mulungu amadana kwambiri ndi aliyense wokonda chiwawa.+