Masalimo
BUKU LACHINAYI
(Masalimo 90 – 106)
Pemphero la Mose, munthu wa Mulungu woona.+
Kapena musanakhazikitse dziko lapansi+ ndi malo okhalapo anthu,*+
Inu ndinu Mulungu kuyambira kalekale mpaka kalekale.+
5 Mwawawonongeratu,+ ndipo amangozimiririka ngati maloto.+
M’mawa amakhala ngati msipu wobiriwira umene watsitsimuka.+
8 Zolakwa zathu mwaziika patsogolo panu,+
Ndipo machimo athu obisika* ali patsogolo pa nkhope yanu yowala.+
9 Pakuti masiku athu onse atha chifukwa cha mkwiyo wanu.+
Zaka zathu zafika kumapeto ngati mpweya wotuluka m’mphuno pousa moyo.+
10 Masiku a moyo wathu amangokwana zaka 70,+
Ndipo ngati tili ndi mphamvu yapadera amakwana zaka 80.+
Koma ngakhale zili choncho, amangodzaza ndi mavuto ndi zopweteka.+
Pakuti masiku amene timakhala ndi moyo amatha mwamsanga ndipo timachoka mofulumira.+
11 Ndani angadziwe kukula kwa ukali wanu,+
Ndi kukula kwa mkwiyo wanu kumene kumafanana ndi ulemu umene muyenera kulandira?+
13 Bwererani kwa ife, inu Yehova!+ Kodi mudzatenga nthawi yaitali bwanji musanabwerere kwa ife?+
Timvereni chisoni ife atumiki anu.+
14 M’mawa mutikhutiritse ndi kukoma mtima kwanu kosatha,+
Kuti tifuule mokondwera ndi kuti tikhale osangalala masiku onse a moyo wathu.+