Yohane
15 “Ine ndine mtengo wa mpesa weniweni,+ ndipo Atate wanga ndiye mlimi.+ 2 Nthambi iliyonse mwa ine yosabala zipatso amaidula,+ ndipo iliyonse yobala zipatso amaiyeretsa mwa kuitengulira+ kuti ibale zipatso zambiri.+ 3 Inu ndinu oyera kale chifukwa cha mawu amene ine ndalankhula kwa inu.+ 4 Khalani ogwirizana ndi ine, inenso ndikhala wogwirizana ndi inu.+ Nthambi singabale zipatso payokha, pokhapokha ngati ndi yolumikizikabe kumpesawo. Chimodzimodzi inunso, simungabale zipatso mukapanda kukhala olumikizika kwa ine.+ 5 Ine ndine mtengo wa mpesa, inu ndinu nthambi zake. Amene ali wolumikizika kwa ine, inenso n’kukhala wolumikizika kwa iye, ameneyo amabala zipatso zochuluka,+ chifukwa simungathe kuchita kalikonse popanda ine. 6 Ngati munthu sakhala wolumikizika kwa ine, amaponyedwa kunja monga nthambi ndipo amauma. Nthambi zoterozo anthu amazisonkhanitsa ndi kuziponya pamoto ndipo zimapsa.+ 7 Ngati mukhala ogwirizana ndi ine ndipo mawu anga akakhala mwa inu, mukhoza kupempha chilichonse chimene mukufuna ndipo chidzachitika kwa inu.+ 8 Atate amalemekezeka mukapitiriza kubala zipatso zambiri ndi kusonyeza kuti mulidi ophunzira anga.+ 9 Monga Atate wakondera ine,+ inenso kukonda inu, inunso khalanibe m’chikondi changa. 10 Mukasunga malamulo anga,+ mudzakhalabe m’chikondi changa, monga mmene ine ndasungira malamulo a Atate+ ndi kukhalabe m’chikondi chake.
11 “Ndalankhula zinthu izi kwa inu, kuti chimwemwe changa chikhale mwa inu, ndi kuti chimwemwe chanu chisefukire.+ 12 Lamulo langa ndi ili, mukondane monga mmene inenso ndakukonderani.+ 13 Palibe amene ali ndi chikondi chachikulu kuposa cha munthu amene wapereka moyo wake chifukwa cha mabwenzi ake.+ 14 Mupitiriza kukhala mabwenzi anga mukamachita zimene ndikukulamulani.+ 15 Sindikutchanso inu kuti akapolo, chifukwa kapolo sadziwa zimene mbuye wake amachita. Koma ndakutchani mabwenzi,+ chifukwa zonse zimene ndamva kwa Atate wanga ndakudziwitsani.+ 16 Inu simunandisankhe ine, koma ine ndinakusankhani. Ndinakuikani kuti mupitirize kubala zipatso zochuluka,+ ndi kutinso zipatso zanuzo zisathe, kuti chilichonse chimene mungapemphe Atate m’dzina langa akupatseni.+
17 “Ndikukulamulani zinthu izi, kuti muzikondana.+ 18 Ngati dziko likudana nanu, mukudziwa kuti linadana ndi ine lisanadane ndi inu.+ 19 Mukanakhala mbali ya dziko, dziko likanakukondani monga mbali yake.+ Koma popeza simuli mbali ya dzikoli,+ koma ine ndinakusankhani kuchokera m’dziko, pa chifukwa chimenechi dziko likudana nanu.+ 20 Kumbukirani mawu amene ndinakuuzani aja, kapolo sali wamkulu kuposa mbuye wake. Ngati anazunza ine, inunso adzakuzunzani.+ Ngati asunga mawu anga, adzasunganso anu. 21 Koma adzakuchitirani zonsezi chifukwa cha dzina langa, chifukwa amene anandituma ine sakumudziwa.+ 22 Ndikanapanda kubwera kudzalankhula nawo, akanakhala opanda tchimo,+ koma tsopano alibe chodzilungamitsira pa tchimo lawo.+ 23 Wodana ndi ine amadananso ndi Atate wanga.+ 24 Ndikanapanda kuchita pakati pawo ntchito zimene wina aliyense sanachitepo,+ akanakhala opanda tchimo,+ koma tsopano aona ndipo adana nane, ndi kudananso ndi Atate wanga.+ 25 Zili choncho kuti mawu olembedwa m’Chilamulo akwaniritsidwe. Mawu ake ndi akuti, ‘Anadana nane popanda chifukwa.’+ 26 Akadzafika mthandizi amene ndidzamutumiza kuchokera kwa Atate,+ amene ndi mzimu wa choonadi wochokera kwa Atate, ameneyo adzandichitira umboni,+ 27 ndipo inunso mudzachitira umboni,+ chifukwa mwakhala nane kuchokera pa chiyambi.