Mika
7 Tsoka kwa ine,+ chifukwa ndakhala ngati munthu wanjala amene sanapeze zipatso kuti adye.+ Ndakhala ngati munthu amene sanapeze nkhuyu zoyambirira zimene anali kuzilakalaka, nthawi yokolola zipatso za m’chilimwe* ndi mphesa itatha.+ 2 Anthu okhulupirika atha padziko lapansi, ndipo pakati pa anthu palibe munthu wowongoka mtima.+ Onse amadikirira anzawo kuti akhetse magazi.+ Aliyense amasaka m’bale wake ndi ukonde.+ 3 Manja awo amachita zoipa ndipo amazichita bwino kwambiri.+ Kalonga amalamula kuti amupatse mphatso, ndipo woweruza amalandira chiphuphu poweruza.+ Munthu wotchuka amangolankhula zolakalaka za mtima wake+ ndipo onsewa amakonzera limodzi chiwembu. 4 Munthu wabwino kwambiri pakati pawo ali ngati chitsamba chaminga, ndipo munthu wowongoka mtima kwambiri pakati pawo ndi woipa kwambiri kuposa mpanda wa mitengo yaminga.+ Tsiku limene mudzapatsidwe chilango, limene alonda anu ananena, lidzafika ndithu.+ Pa tsikulo anthu adzathedwa nzeru.+
5 Musamakhulupirire anzanu. Musamadalire mnzanu wapamtima.+ Samala zonena zako polankhula ndi amene umagona naye pafupi.+ 6 Pakuti mwana wamwamuna akunyoza bambo ake. Mwana wamkazi akuukira mayi ake+ ndipo mkazi wokwatiwa akuukira apongozi ake aakazi.+ Adani ake a munthu ndi anthu a m’banja lake.+
7 Koma ine ndidzadikirira Yehova.+ Ndidzayembekezera moleza mtima Mulungu wa chipulumutso changa.+ Mulungu wanga adzandimvera.+
8 Iwe mdani wanga,+ usasangalale chifukwa cha zimene zandichitikira. Ngakhale kuti ndagwa, ndidzadzuka ndithu.+ Ngakhale kuti ndili mumdima,+ Yehova adzakhala kuwala kwanga.+ 9 Mkwiyo waukulu wa Yehova ndiupirira chifukwa ndamuchimwira.+ Ndiupirirabe kufikira ataweruza mlandu wanga mondikomera ndi kundichitira chilungamo.+ Iye adzandipititsa pamalo owala ndipo ndidzaona kulungama kwake.+ 10 Mdani wanga adzaona zimenezi, ndipo amene anali kunena kuti: “Yehova Mulungu wako ali kuti?”+ adzachita manyazi.+ Maso anga adzamuyang’ana.+ Iye adzakhala malo opondedwapondedwa ngati matope a mumsewu.+
11 Pa tsiku lomanga mpanda wako wamiyala lamulo lokhudza iwe lidzachotsedwa.*+ 12 Pa tsiku limenelo anthu adzabwera kwa iwe kuchokera ku Asuri ndi kumizinda ya Iguputo. Anthu ochokera ku Iguputo mpaka ku Mtsinje*+ adzabwera kwa iwe. Adzabwera kuchokera m’malo onse apakati pa nyanja imodzi ndi nyanja ina, komanso pakati pa phiri limodzi ndi phiri lina.+ 13 Dzikoli lidzakhala bwinja chifukwa cha zochita za anthu okhala mmenemo ndi zotsatirapo za zochita zawozo.+
14 Weta anthu ako ndi ndodo yako.+ Weta gulu la nkhosa zomwe ndi cholowa chako, zimene zinali kukhala zokhazokha m’nkhalango pakati pa mitengo ya zipatso.+ Uzilole kuti zikadyere ku Basana ndi ku Giliyadi+ ngati mmene zinali kuchitira masiku akale.+
15 “Anthu inu ndidzakusonyezani zinthu zodabwitsa ngati mmene ndinachitira m’masiku amene munali kuchokera ku Iguputo.+ 16 Anthu a mitundu ina adzaona zodabwitsazo ndipo adzachita manyazi ngakhale kuti ali ndi mphamvu.+ Adzagwira pakamwa+ ndipo makutu awo adzagontha. 17 Adzanyambita fumbi ngati njoka.+ Adzatuluka m’malo awo obisalamo+ ngati zokwawa zapadziko lapansi ali ndi mantha. Adzabwera kwa Yehova Mulungu akunjenjemera ndipo adzachita nanu mantha.”+
18 Kodi pali Mulungu winanso wofanana ndi inu+ amene amakhululukira zolakwa+ ndi machimo a anthu ake otsala omwe ndi cholowa chake?+ Inu simudzakhalabe wokwiya mpaka kalekale, pakuti kusonyeza kukoma mtima kosatha kumakusangalatsani.+ 19 Inu mudzatichitiranso chifundo+ ndipo mudzapondaponda zolakwa zathu.+ Machimo athu onse mudzawaponya pakati pa nyanja yozama.+ 20 Zonse zimene munanena kwa Yakobo zinali zoona ndipo Abulahamu munamusonyeza kukoma mtima kosatha. Ifenso mudzatichitira zomwezo chifukwa n’zimene munalonjeza makolo athu kalekale.+