1 Akorinto
5 Mbiri yamvekatu kuti pakuchitika dama*+ pakati panu, ndipo dama lake ndi loti ngakhale anthu a mitundu ina sachita. Akuti mwamuna wina watengana ndi mkazi wa bambo ake.+ 2 Kodi mukudzitukumula,+ m’malo mwa kumva chisoni,+ kuti munthu amene anachita zimenezi achotsedwe pakati panu?+ 3 Ineyo pandekha, ngakhale kuti mwa thupi sindili kumeneko koma mu mzimu ndili komweko, ndamuweruza kale+ ndithu munthu amene wachita zimenezi, ngati kuti ndinali nanu kumeneko. 4 Ndaweruza kuti m’dzina la Ambuye wathu Yesu, mukakumana pamodzi, komanso ndi mzimu wanga ndi mphamvu ya Ambuye wathu Yesu,+ 5 mupereke munthu ameneyu kwa Satana+ kuti thupilo liwonongedwe, n’cholinga choti mzimuwo+ upulumutsidwe m’tsiku la Ambuye.+
6 Chimene mukudzitamira+ si chabwino ayi. Kodi simukudziwa kuti chofufumitsa chaching’ono chimafufumitsa+ mtanda wonse?+ 7 Chotsani chofufumitsa chakalecho, kuti mukhale mtanda watsopano,+ popeza ndinu opanda chofufumitsa. Pakuti Khristu+ waperekedwa+ monga nsembe yathu ya pasika.+ 8 Chotero tiyeni tichite chikondwererochi,+ osati ndi chofufumitsa chakale,+ kapena chofufumitsa+ choimira zoipa ndi uchimo,+ koma ndi mikate yopanda chofufumitsa yoimira kuona mtima ndi choonadi.+
9 M’kalata yanga ndinakulemberani kuti muleke kuyanjana ndi anthu adama. 10 Sindikutanthauza kuti muzipeweratu adama+ a m’dzikoli,+ kapena aumbombo ndi olanda, kapena opembedza mafano ayi. Kuti muchite zimenezo, ndiye mungafunikire kutuluka m’dzikomo.+ 11 Koma tsopano ndikukulemberani kuti muleke kuyanjana+ ndi aliyense wotchedwa m’bale, amene ndi wadama, kapena waumbombo,+ kapena wopembedza mafano, wolalata, chidakwa,+ kapena wolanda, ngakhale kudya naye munthu wotereyu ayi. 12 Nanga kuweruza anthu amene ali kunja*+ ndi ntchito yanga ngati? Kodi inu si paja mumaweruza amene ali mkati,+ 13 ndipo Mulungu amaweruza amene ali kunja?+ “M’chotseni pakati panu munthu woipayo.”+