Yohane
20 Tsiku loyamba+ la mlunguwo, Mariya Mmagadala anabwera kumanda achikumbutsowo m’mawa kwambiri, kudakali mdima, ndipo anaona kuti mwala wachotsedwa kale pamanda achikumbutsowo.+ 2 Pamenepo iye anathamanga ndi kukafika kwa Simoni Petulo ndi kwa wophunzira wina,+ amene Yesu anali kumukonda kwambiri uja. Iye anawauza kuti: “Ambuye awachotsa m’manda achikumbutso+ aja, ndipo sitikudziwa kumene awaika.”
3 Pamenepo Petulo+ ndi wophunzira wina uja ananyamuka kupita kumanda achikumbutsowo. 4 Onse awiri anayambira pamodzi kuthamanga, koma wophunzira winayo anapitirira Petulo ndi liwiro lalikulu ndipo anali woyambirira kukafika kumanda achikumbutsowo. 5 Atawerama ndi kuyang’anitsitsa, anangoona nsalu zokulungira mtembo zokha zija zili pansi,+ koma sanalowe mkatimo. 6 Kenako Simoni Petulo anafikanso m’mbuyo mwake, ndipo analowa m’manda achikumbutsowo. Mmenemo anaona nsalu zokulungira mtembozo zili pansi.+ 7 Anaonanso nsalu ina imene anamukulungira kumutu ataipindapinda ndi kuiika payokha. Imeneyi sinaikidwe pamodzi ndi nsalu zokulungira mtembozo. 8 Pamenepo, wophunzira winayo, amene anali woyambirira kufika kumanda achikumbutso uja analowanso mkatimo, ndipo anaona ndi kukhulupirira zimene Mariya anawauza. 9 Iwo anali asanazindikire malemba akuti Yesu ayenera kuuka kwa akufa.+ 10 Pamenepo ophunzirawo anabwerera kunyumba kwawo.
11 Koma Mariya anatsala atangoima panja pafupi ndi manda achikumbutsowo akulira. Akulira choncho, anawerama kuti aone m’manda achikumbutsowo. 12 Atatero, anaona angelo awiri+ ovala zoyera, mmodzi atakhala pansi kumutu, winanso atakhala pansi kumiyendo, pamalo amene panagona mtembo wa Yesu. 13 Iwo anamufunsa kuti: “Mayi iwe, n’chifukwa chiyani ukulira?” Iye anati: “Atenga Ambuye wanga, ndipo sindikudziwa kumene awaika.” 14 Atanena zimenezi, anatembenuka ndi kuona Yesu ali chilili, koma sanam’zindikire kuti ndi Yesu.+ 15 Ndiyeno Yesu anafunsa mayiyo kuti: “Mayi iwe, n’chifukwa chiyani ukulira? Kodi Ukufuna ndani?”+ Poganiza kuti ndi wosamalira mundawo, iye anamuyankha kuti: “Bambo, ngati mwamuchotsa ndinu, ndiuzeni chonde kumene mwamuika, ndipo ine ndikamutenga.” 16 Pamenepo Yesu anati: “Mariya!”+ Pamene anatembenuka, ananena kwa iye m’Chiheberi kuti: “Rab·boʹni!”+ (kutanthauza kuti “Mphunzitsi!”) 17 Yesu anati: “Usandikangamire. Pakuti sindinakwerebe kwa Atate. Koma pita kwa abale anga+ ukawauze kuti, ‘Ine ndikukwera kwa Atate+ wanga ndi Atate wanu, kwa Mulungu wanga+ ndi Mulungu wanu.’”+ 18 Mariya Mmagadala anafika ndi kuuza ophunzira uthengawo. Anati: “Ambuye ndawaona ine!” Ndipo anawauza zimene iye anamuuza zija.+
19 Pa tsiku limenelo, tsiku loyamba la mlunguwo,+ ophunzirawo anasonkhana pamodzi madzulo. Iwo anali atakhoma zitseko m’nyumba imene analimo chifukwa choopa+ Ayuda, ndipo Yesu anafika+ n’kuimirira pakati pawo ndi kunena kuti: “Mtendere ukhale nanu.”+ 20 Atanena zimenezi, anawaonetsa manja ake ndi pambali pa mimba paja.+ Pamenepo ophunzirawo anasangalala+ poona Ambuyewo. 21 Kenako Yesu anawauzanso kuti: “Mtendere ukhale nanu. Mmene Atate ananditumira,+ inenso ndikutumani.”+ 22 Atanena zimenezi, anauzira mpweya pa iwo ndi kuwauza kuti: “Landirani mzimu woyera.+ 23 Mukakhululukira munthu amene wachita tchimo,+ ndiye kuti Mulungu wamukhululukira kale. Koma mukapanda kukhululukira munthu amene wachita tchimo, ndiye kuti Mulungu sanamukhululukire.”+
24 Koma Tomasi,+ wotchedwa Didimo, mmodzi wa ophunzira 12 aja sanali pamodzi nawo pamene Yesu anafika. 25 Choncho ophunzira enawo anamuuza kuti: “Ife tawaona Ambuye!” Koma iye anati: “Ndithu ndikapanda kuona mabala a misomali m’manja mwawo ndi kuika chala changa m’mabala a misomaliwo, ndiponso kuika dzanja langa m’mbali mwa mimba yawo,+ ine sindikhulupirira ayi.”+
26 Tsopano patapita masiku 8, ophunzira akewo analinso m’nyumba, ndipo Tomasi anali nawo pamodzi. Yesu anafika ngakhale kuti zitseko zinali zokhoma. Iye anaimirira pakati pawo ndi kunena kuti: “Mtendere ukhale nanu.”+ 27 Kenako anauza Tomasi kuti: “Ika chala chako apa, ndiponso ona m’manja mwangamu. Gwiranso ndi dzanja lako+ m’mbali mwa mimba yangamu, kuti usakhalenso wosakhulupirira, koma wokhulupirira.” 28 Poyankha Tomasi anati: “Mbuyanga ndi Mulungu wanga!”+ 29 Yesu anamufunsa kuti: “Kodi wakhulupirira chifukwa wandiona? Odala ndi amene amakhulupirira ngakhale sanaone.”+
30 Kunena zoona, Yesu anachita zizindikiro zinanso zambiri pamaso pa ophunzirawo, zimene sizinalembedwe mumpukutu uno.+ 31 Koma izi zalembedwa+ kuti mukhulupirire kuti Yesu alidi Khristu Mwana wa Mulungu, ndi kutinso, mwa kukhulupirira,+ mukhale ndi moyo m’dzina lake.