7Kenako Yehova anauza Nowa kuti: “Lowa mʼchingalawacho, iwe ndi banja lako, chifukwa iwe ndi amene ndakuona kuti ndiwe wolungama pakati pa mʼbadwo uwu.+
7 Chifukwa cha chikhulupiriro, Nowa+ atachenjezedwa ndi Mulungu za zinthu zimene zinali zisanaoneke,+ anasonyeza kuopa Mulungu ndipo anamanga chingalawa+ kuti banja lake lipulumukiremo. Chifukwa cha chikhulupiriro, anatsutsa dziko+ ndipo anaonedwa kuti ndi wolungama chifukwa cha chikhulupirirocho.