-
Genesis 47:29, 30Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
29 Tsopano nthawi yakuti Isiraeli amwalire inayandikira.+ Ndiye anaitana mwana wake Yosefe nʼkumuuza kuti: “Ngati ungandikomere mtima, ika dzanja lako pansi pa ntchafu yanga. Ulumbire kuti udzandisonyeza chikondi chokhulupirika komanso kuti udzakhala wokhulupirika kwa ine. Chonde, usadzandiike mʼmanda ku Iguputo kuno.+ 30 Ndikadzamwalira,* udzandinyamule kuchoka ku Iguputo kuno nʼkukandiika mʼmanda a makolo anga.”+ Yosefe anayankha kuti: “Ndidzachitadi mogwirizana ndi zimene mwanena.”
-