26 Tsopano mʼdzikomo munagwa njala yaikulu ngati imene inagwa mʼmasiku a Abulahamu.+ Choncho Isaki anapita kwa Abimeleki, mfumu ya Afilisiti, ku Gerari. 2 Ndiyeno Yehova anaonekera kwa iye nʼkumuuza kuti, “Usapite ku Iguputo. Ukhale mʼdziko limene ndikusonyeze.